Jeremiah 52:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa chaka cha 23 cha ufumu wa Nebukadinezara, Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda oteteza mfumu uja adatenga ukapolo Ayuda 745. Onse pamodzi otengedwa ukapolo adakwanira 4,600.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chaka cha makumi awiri ndi zitatu cha Nebukadinezara Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende Ayuda mazana asanu ndi awiri kudza makumi anai ndi asanu; anthu onse anali zikwi zinai kudza mazana asanu ndi limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mʼchaka cha 23 cha ulamuliro wa Nebukadinezara, Nebuzaradani, mtsogoleri wa ankhondo a mfumu anagwira Ayuda 745 kupita ku ukapolo. Onse pamodzi analipo anthu 4,600.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
caka ca makumi awiri ndi zitatu ca Nebukadirezara Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende Ayuda mazana asanu ndi awiri kudza makumi anai ndi asanu; anthu onse anali zikwi zinai kudza mazana asanu ndi limodzi.