Jeremiah 52:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa chaka cha 37 cha ukapolo wa Yehoyakimu, mfumu ya ku Yuda, tsiku la 25 la mwezi wa 12, Evili-Merodaki, mfumu ya ku Babiloni adangoti ataloŵa ufumu, adakomera mtima Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, namtulutsa m'ndende.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri cha undende wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi iwiri, tsiku la makumi awiri ndi asanu la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya ku Babiloni anaweramutsa mutu wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, namtulutsa iye m'ndende;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka chimene Evili-Merodaki analowa ufumu wa Babuloni, iye anakomera mtima Yehoyakini mfumu ya ku Yuda, namutulutsa mʼndende. Izi zinachitika pa tsiku la 25 la mwezi wa khumi ndi chiwiri zitatha zaka 37 chitengedwere Yehoyakimu ku ukapolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali caka ca makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri ca undende wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi iwiri, tsiku la makumi awiri ndi asanu la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya ku Babulo anaweramutsa mutu wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, namturutsa iye m'ndende;