Jeremiah 52:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye pa chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wa Zedekiyayo, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adabwera ndi ankhondo ake onse kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu. Adauzinga ndi zithando zankhondo ponseponse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panaoneka chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wake mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anafika, iye ndi nkhondo yake, kuti amenyane ndi Yerusalemu, ndipo anammangira zithando; ndipo anammangira malinga pozungulira pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho mʼchaka cha chisanu ndi chinayi cha ulamuliro wa Zedekiya, mwezi wakhumi, pa tsiku la khumi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anabwera ndi ankhondo ake onse kudzathira nkhondo Yerusalemu. Anamanga misasa ndi mitumbira yankhondo kunja kuzungulira mzindawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panaoneka caka cacisanu ndi cinai ca ufumu wace mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo anafika, iye ndi nkhondo yace, kuti amenyane ndi Yerusalemu, ndipo anammangira zitando; ndipo anammangira malinga pozungulira pace.