Jeremiah 52:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
malinga a mzindawo adabooledwa. Pamenepo ankhondo onse adathaŵa mumzindamo usiku, kutulukira pa chipata cha pakati pa makoma aŵiri, pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababiloni anali atauzinga mzindawo. Ndipo adathaŵira ku Araba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anaboola mudzi, ndipo anathawa amuna onse a nkhondo, natuluka m'mudzi usiku pa njira ya kuchipata cha pakati pa makoma awiri, imene inali pa munda wa mfumu; Ababiloni alikumenyana ndi mudzi pozungulira pake, ndipo anapita njira ya kuchidikha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono linga la mzindawo linabowoledwa, ndipo ankhondo onse anathawa. Iwo anatuluka mu mzindamo usiku kudzera pa chipata cha pakati pa makoma awiri a pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababuloni anali atazinga mzindawo. Ndipo anathawira ku Araba,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anaboola mudzi, ndipo anathawa amuna onse a nkhondo, naturuka m'mudzi usiku pa njira ya kucipata ca pakati pa makoma awiri, imene inali pa munda wa mfumu; Akasidi alikumenyana ndi mudzi pozungulira pace, ndipo anapita njira ya kucidikha.