Jeremiah 6:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Chauta, sindingathenso kudzimanga kuti usatulukire kunja. Chauta akuti, “Mkwiyo umenewu ukauthire pa ana oyenda mu mseu, ndi pa achinyamata kumene amasonkhanira. Mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, ngakhale aimvi ndi okalamba kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake ndadzala ndi ukali wa Yehova; ndalema ndi kudzikaniza; tsanulirani pa ana a pabwalo, ndi pa masonkhano a anyamata, pakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, okalamba ndi iye amene achuluka masiku ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ine ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Yehova, ndipo ndatopa ndi kusunga mkwiyo wa Yehova. Yehova anandiwuza kuti, “Tsono ndidzawutulutsira mkwiyo umenewu pa ana oyenda mʼmisewu ndi pa achinyamata amene asonkhana pamodzi; pakutinso mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, pamodzi ndi okalamba amene ali ndi zaka zochuluka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace ndadzala ndi ukali wa Yehova; ndalema ndi kudzikaniza; tsanulirani pa ana a pabwalo, ndi pa masonkhano a anyamata, pakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi wace adzatengedwa, okalamba ndi iye amene acuruka masiku ace.