Jeremiah 6:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi akamachita zonyansa, amachita manyazi ngati? Iyai, sachita manyazi mpang'ono pomwe. Sadziŵa nkugwetsa nkhope komwe. Nchifukwa chake adzagwera pakati pa anzao amene adagwa kale. Adzagweratu pa tsiku limene ndidzaŵalanga!” Akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita chonyansa? Iai, sanakhale konse ndi manyazi, sanathe kunyala; chifukwa chake adzagwa mwa iwo akugwa; panthawi pamene ndidzafika kwa iwo, adzagwetsedwa, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazo? Ayi, sachita manyazi ndi pangʼono pomwe; sadziwa ndi kugwetsa nkhope komwe. Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale; adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalange,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi anakhala ndi manyazi pamene anacita conyansa? lai, sanakhala konse ndi manyazi, sanathe kunyala; cifukwa cace adzagwa mwa iwo akugwa; panthawi pamene ndidzafika cwa iwo, aclzagwetsedwa, ati Yehova.