Jeremiah 6:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tamvani inu okhala pa dziko lapansi, anthuwo ndidzaŵaononga. Komatu zimenezo nzotsatira za kunyenga kwao, chifukwa sadamvere mau anga ndipo sadamvere malamulo anga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tamva, dziko lapansi iwe; taona, Ine ndidzatengera choipa pa anthu awa, chipatso cha maganizo ao, pakuti sanamvere mau anga, kapena chilamulo changa, koma wachikana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Imvani, inu anthu okhala pa dziko lapansi, ndikubweretsa masautso pa anthu awa. Zimenezi ndi mphotho ya ntchito zawo. Iwowa sanamvere mawu anga ndipo anakana lamulo langa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tamva, dziko lapansi iwe; taona, Ine ndidzatengera coipa pa anthu awa, cipatso ca maganizo ao, pakuti sanamvera mau anga, kapena cilamulo canga, koma wacikana.