Jeremiah 6:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake anthu ameneŵa ndidzaŵaikira zoŵakhumudwitsa. Atate ndi ana ao aamuna, anansi ndi abwenzi ao, onsewo adzaonongeka.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake atero Yehova, Taona, ndidzaikira anthuwa zophunthwitsa; ndipo atate ndi ana adzakhumudwa nazo pamodzi; munthu ndi mnzake adzatayika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yehova akuti, “Ndidzayika zokhumudwitsa pamaso pa anthu awa. Abambo ndi ana awo aamuna onse adzapunthwa ndi kugwa; anansi awo ndi abwenzi awo adzawonongeka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace atero Yehova, Taona, ndidzaikira anthuwa zopunthwitsa; ndipo atate ndi ana adzakhumudwa nazo pamodzi; munthu ndi mnzace adzatayika.