Jeremiah 6:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atenga mauta ndi mikondo, ndi anthutu ankhalwe ndi opanda chifundo. Phokoso lao lili ngati mkokomo wa nyanja. Akwera pa akavalo, akonzekera ngati munthu wankhondo, akudzamenyana nawe, iwe Ziyoni.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe chifundo; mau ao aphokosera ngati nyanja, akwera pa akavalo; aguba monga anthu ofuna kumenyana nkhondo ndi iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atenga mauta ndi mikondo; ndi anthu ankhanza ndi opanda chifundo. Phokoso lawo lili ngati mkokomo wa nyanja. Akwera pa akavalo awo ndipo akonzekera ngati anthu ankhondo, kudzakuthirani nkhondo anthu a ku Ziyoni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe cifundo; mau ao aphokosera ngati nyanja, akwera pa akavalo; aguba monga anthu ofuna kumenyana nkhondo ndi iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni.