Jeremiah 6:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
A ku Yerusalemu akuti, “Mbiri ya iwowo taimva, m'nkhongono mwati zii. Nkhaŵa yatigwira, ndipo tikumva ululu wonga wa mkazi panthaŵi yake yochira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tamva ife mbiri yake; manja athu alefuka, yatigwira nkhawa ndi zowawa ngati za mkazi wobala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
A ku Ziyoni akuti “Ife tamva mbiri yawo, ndipo manja anthu alefukiratu. Nkhawa yatigwira, ndipo tikumva ululu ngati mayi pa nthawi yake yochira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tamva ife mbiri yace; manja athu alefuka, yatigwira nkhawa ndi zowawa ngati za mkazi wobala.