Jeremiah 6:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu anthu anga, valani ziguduli, gubuduzikani pa phulusa. Lirani kwamphamvu, ngati munthu wolira mwana wake mmodzi yekha, pakuti mwadzidzidzi woononga adzabwera kudzakuphani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, udziveke ndi chiguduli, ndi kuvimvinika m'phulusa; ulire maliro ngati a mwana wamwamuna wa yekha, kulira kowawa koposa; pakuti wakufunkha adzatifikira ife motidzidzimutsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu anthu anga, valani ziguduli ndipo gubudukani pa phulusa; lirani mwamphamvu ngati munthu wolirira mwana wake mmodzi yekha, pakuti mwadzidzidzi wowonongayo adzabwera kudzatipha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, udzibveke ndi ciguduli, ndi kubvimbvinika m'phulusa; ulire maliro ngati a mwana wamwamuna wa yekha, kulira kowawa koposa; pakuti wakufunkha adzatifikira ife motidzidzimutsa.