Jeremiah 6:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mvukuto zikuuzira kwambiri, mtovu wasungunuka ndi moto. Koma ntchito yosungunulayo sikupindula, chifukwa choti dothi loipa silikuchokapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mvukuto yatenthedwa ndi moto; mtovu watha ndi moto wa ng'anjo; ayenga chabe; pakuti oipa sachotsedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Moto mu mvukuto ukuyaka kwambiri; mtovu watha kusungunuka ndi moto. Koma ntchito yosungunulayo sikupindula chifukwa zoyipa sizikuchokapo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mbvukuto yatenthedwa ndi moto; mthobvu watha ndi moto wa ng'anjo; ayenga cabe; pakuti oipa sacotsedwa.