Jeremiah 6:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga momwe chitsime chimasungira madzi ake, ndimonso m'mene mzindawo umasungira zoipa zake. Zimene mukumva ndi za chiwonongeko ndi za nkhondo. Ndikuwonamonso matenda ndi zilonda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga kasupe atulutsa madzi ake, chomwecho atulutsa zoipa zake; chiwawa ndi kufunkha zimveka m'kati mwake; pamaso panga masiku onse pali kulira ndi mabala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga momwe chitsime chimatulutsira madzi ndi mmenenso Yerusalemu amatulutsira zoyipa zake. Chiwawa ndi chiwonongeko ndi zomwe zimamveka mu mzindamo; nthenda yake ndi mabala ake ndimaziona nthawi zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga kasupe aturutsa madzi ace, camweco aturutsa zoipa zace; ciwawa ndi kufunkha zimveka m'kati mwace; pamaso panga masiku onse pali kulira ndi mabala.