Jeremiah 6:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe Yerusalemu, tengapo phunziro, kuwopa kuti chikondi changa pa iwe chingathe, ndipo ndingakusandutse dziko lachipululu, dziko lopanda anthu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ulangizidwe, Yerusalemu, ungakuchokere moyo wanga, ndingakuyese iwe bwinja, dziko losakhalamo anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe Yerusalemu, tengapo phunziro, kuopa kuti chikondi changa pa iwe chingakuchokere ndi kusandutsa dziko lako kukhala bwinja mopanda munthu wokhalamo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ulangizidwe, Yerusalemu, ungakucokere moyo wanga, ndingakuyese iwe bwinja, dziko losakhalamo anthu.