Jeremiah 6:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mau a Chauta Wamphamvuzonse akuti, “Akunkheni ndi kuŵalanda zonse anthu otsala a Aisraele, monga momwe anthu amachitira, populula mphesa ku nthambi zake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova wa makamu atero, Adzakunkha otsalira a Israele monga mpesa; bweza dzanja lako monga wakutchera mphesa m'madengu ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse anandiwuza kuti, “Adani adzawakunkha ndithu anthu otsala a Israeli, monga momwe amachitira populula mphesa. Tsono iwe yesetsa kupulumutsa amene ungathe monga mmene amachitira munthu wokolola mphesa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova wa makamu atero, Adzakunkha otsalira a Israyeli monga mpesa; bweza dzanja lako monga wakuchera mphesa m'mitanga yace.