Jeremiah 7:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munkachita zoipa zonsezi, mudakana kundimvera nditakulankhulani kosalekeza, ndipo simudayankhe pamene ndidakuitanani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, chifukwa munachita ntchito zonsezi, ati Yehova, ndipo ndinanena kwa inu, ndi kuuka mamawa ndi kunena, koma simunamva; ndipo ndinakuitanani inu, koma simunayankha;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono popeza munkachita zonsezi, ngakhale Ine kukuyankhulani koma inu osamvera, kukuyitanani koma inu osayankha,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, cifukwa munacita nchito zonsezi, ati Yehova, ndipo ndinanena kwa inu, ndi kuuka mamawa ndi kunena, koma simunamva; ndipo ndinakuitanani inu, koma simunayankha;