Jeremiah 7:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake zomwe ndidachita ku Silo, ndidzachitanso ku Nyumba ino, imene imadziŵika ndi dzina langa, malo amene inu mumaŵakhulupirira, malo amene ndidakupatsani inu pamodzi ndi makolo anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake ndidzaichitira nyumba iyi, imene itchedwa dzina langa, imene mukhulupirirayi, ndipo ndidzachitira malo amene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, monga ndinachitira Silo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
choncho ndidzachita pa Nyumba imene imadziwika ndi Dzina langayi, Nyumba ya Yehova imene mumayidalira, malo amene ndinapereka kwa inu ndi makolo anu, zomwe ndinachita ku Silo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace ndidzaicitira nyumba iyi, imene ichedwa dzina langa, imene mukhulupirirayi, ndipo ndidzacitira malo amene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, monga ndinacitira Silo.