Jeremiah 7:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana akutolera nkhuni, atate akusonkha moto, akazi akukanda ufa kuti aphike makeke, kuchitira ulemu amene amati ndi mfumukazi yakumwamba. Iwowo amathira nsembe yazakumwa kwa milungu ina, kuti andipsetse mtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ana atola nkhuni, atate akoleza moto, akazi akanyanga ufa, kuti aumbe mikate ya mfumu yaikazi ya kumwamba, athirire milungu ina nsembe yothira, kuti autse mkwiyo wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana akutorera nkhuni, abambo akusonkha moto, ndipo amayi akukanda ufa kuti aphike makeke oti akapereke nsembe kwa mfumukazi yazakumwamba. Iwo amathira nsembe ya zakumwa kwa milungu ina kuti andipsetse mtima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ana atola nkhuni, atate akoleza moto, akazi akanyanga ufa, kuti aumbe mikate ya mfumu yaikazi ya kumwamba, athirire milungu yina nsembe yothira, kuti autse mkwiyo wanga.