Jeremiah 7:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ima pa chipata cha Nyumba ya Chauta ndipo kumeneko ukalalike kuti: Imvani mau a Chauta, inu nonse anthu a ku Yuda, amene mumaloŵa pa chipata ichi kudzapembedza Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ima m'chipata cha nyumba ya Yehova, lalikira m'menemo mau awa, ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, inu nonse a Yuda, amene alowa m'zipata izi kuti mugwadire Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ima pa chipata cha Nyumba ya Yehova ndipo kumeneko ukalalikire uthenga uwu: “ ‘Imvani mawu a Yehova, inu nonse anthu a ku Yuda amene mumalowa pa chipata ichi kudzapembedza Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ima m'cipata ca nyumba ya Yehova, lalikira m'menemo mau awa, ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, inu nonse a Yuda, amene alowa m'zipata izi kuti mugwadire Yehova.