Jeremiah 7:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma chimene ndidaalamula nchimodzi, ndidati, ‘Mukamandimvera, ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga. Muzitsata malamulo anga onse kuti zinthu zikukomereni!’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma chinthu ichi ndinawauza, kuti, Mverani mau anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga; nimuyende m'njira yonse imene ndakuuzani inu, kuti chikukomereni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
koma ndinawalamula kuti: Mverani Ine, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu ndipo inu mudzakhala anthu anga. Muzitsata zonse zimene ndakulamulirani, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma cinthu ici ndinawauza, kuti, Mverani mau anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga; nimuyende m'njira yonse imene ndakuuzani inu, kuti cikukomereni.