Jeremiah 7:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Meta tsitsi lako, ndipo ulitaye. Ulire kwambiri pa zitunda zopanda zomera, poti Chauta waukana mbadwo uwu umene wamkwiyitsa. Anthu amenewo Iye waŵasiyadi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Meta tsitsi lako, iwe Yerusalemu, nulitaye, nukweze maliro pa mapiri oti see; pakuti Yehova wakana ndi kusiya mbadwo umene aukwiyira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono meta tsitsi lako ndi kulitaya. Ulire kwambiri pa zitunda zopanda zomera, pakuti Yehova waukana ndi kuwusiya mʼbado umene wamukwiyitsawu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Senga tsitsi lako, iwe Yerusalemu, nulitaye, nukweze maliro pa mapiri oti se; pakuti Yehova wakana ndi kusiya mbadwo umene aukwiyira.