Jeremiah 7:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Anthu a ku Yuda achita zoipa Ine ndikuwona. Aimika mafano ao onyansa m'Nyumba ino imene imadziŵika ndi dzina langa, ndipo aiipitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ana a Yuda anachita choipa pamaso panga, ati Yehova; naika zonyansa zao m'nyumba yotchedwa dzina langa, kuti alipitse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Anthu a ku Yuda achita zoyipa pamaso panga, akutero Yehova. Ayimika mafano awo onyansa mʼnyumba imene imadziwika ndi Dzina langa ndipo ayipitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ana a Yuda anacita coipa pamaso panga, ati Yehova; naika zonyansa zao m'nyumba yochedwa dzina langa, kuti alipitse.