Jeremiah 7:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amanga nsanja yotchedwa Tofeti m'chigwa cha Benihinomu, kuti atenthereko ana ao aamuna ndi aakazi. Zimenezo sindidalamule konse, ngakhale kuziganiza komwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Namanga akachisi a ku Tofeti, kuli m'chigwa cha mwana wa Hinomu, kuti atenthe m'moto ana ao aamuna ndi aakazi; chimene sindinauza iwo, sichinalowa m'mtima mwanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amanga nsanja yopembedzera Tofeti mʼChigwa cha Hinomu kuti apserezereko ana awo aamuna ndi aakazi. Zimenezi Ine sindinawalamulire ngakhale kuziganizira nʼkomwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Namanga akacisi a ku Tofeti, kuli m'cigwa ca mwana wa Hinomu, kuti atenthe m'moto ana ao amuna ndi akazi; cimene sindinauza iwo, sicinalowa m'mtima mwanga.