Jeremiah 7:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake nthaŵi ikubwera pamene malo ano sadzatchedwanso Tofeti, kapena za Chigwa cha Benihinomu, koma za Chigwa cha Chipheiphe, pakuti anthu akufa adzaŵaika ku Tofeti, chifukwa choti sikudzapezekanso malo owaika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake, taonani, masiku alikudza, ati Yehova, ndipo sadzatchedwanso Tofeti, kapena Chigwa cha mwana wa Hinomu, koma Chigwa cha Kuphera; pakuti adzataya m'Tofeti, kufikira malo akuikamo adzasowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake masiku akubwera, akutero Yehova, pamene anthu sadzawatchulanso malowo Tofeti kapena Chigwa cha Hinomu, koma adzawatchula Chigwa cha Imfa, chifukwa adzakwirira anthu akufa ku Tofeti mpaka osapezekanso malo owayika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace, taonani, masiku alikudza, ati Yehova, ndipo sadzachedwanso Tofeti, kapena Cigwa ca mwana wa Hinomu, koma Cigwa ca Kuphera; pakuti adzataya m'Tofeti, kufikira malo akuikamo adzasowa.