Jeremiah 8:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake akazi ao ndidzaŵapatsa kwa anthu ena, minda yao ndidzaipereka kwa amene aŵagonjetsa. Ndithudi, kuyambira ana ndi akulu omwe, onsewo ali ndi khwinthi la phindu lopeza monyenga. Aneneri ndi ansembe omwe, onsewo ndi onyenga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake ndidzapereka akazi ao kwa ena, ndi minda yao kwa iwo adzalowamo; pakuti onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu asirirasirira; kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita zonyenga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake akazi awo ndidzawapereka kwa amuna ena ndipo minda yawo ndidzayipereka kwa amene adzawagonjetse. Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, onse ali ndi khalidwe lofuna kupeza chuma mwakuba. Aneneri pamodzi ndi ansembe omwe, onse amachita zachinyengo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace ndidzapereka akazi ao kwa ena, ndi minda yao kwa iwo adzalowamo; pakuti onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru asirirasirira; kuyambira mneneri kufikira wansembe onse acita zonyenga.