Jeremiah 8:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu amati, “Chifukwa chiyani tikungokhala? Tiyeni tonse pamodzi tithaŵire ku mizinda yamalinga, tikafere komweko. Chauta, Mulungu wathu, wagamula kuti tiyenera kufa, watimwetsa madzi aululu pakuti tamchimwira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tikhaliranji ife? Tasonkhanani, tilowe m'midzi yamalinga, tikhale chete m'menemo; pakuti Yehova Mulungu wathu watikhalitsa ife chete, natipatsa ife madzi a ndulu timwe, pakuti tamchimwira Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma amati, “Tikukhala pano chifukwa chiyani? Tiyeni tonse pamodzi tithawire ku mizinda yotetezedwa ndi kukafera kumeneko. Pakuti Yehova Mulungu wathu watsimikiza kuti tiyenera kufa. Watipatsa madzi aululu kuti timwe, chifukwa tamuchimwira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tikhaliranji ife? tasonkhanani, tilowe m'midzi yamalinga, tikhale cete m'menemo; pakuti Yehova Mulungu wathu watikhalitsa ife cete, natipatsa ife madzi a ndulu timwe, pakuti tamcimwira Yehova.