Jeremiah 8:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Adani athu aloŵa kale mu mzinda wa Dani. Dziko lonse likunjenjemera ndi kulira kwa akavalo ao. Adani akubwera kudzaononga dzikoli pamodzi ndi zinthu zake zonse. Adzaononganso mzinda ndi onse okhalamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kumina kwa akavalo ake kunamveka ku Dani; dziko lonse linanthunthumira pa kulira kwa akavalo akewo olimba; chifukwa afika, nadya dziko ndi zonse za momwemo; mudzi ndi amene akhalamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kulira kwa ngʼombe zazimuna za mdani kukumveka kuchokera ku Dani; dziko lonse likunjenjemera chifukwa cha kulira kwa akavalowo. Akubwera kudzawononga dziko ndi zonse zimene zili mʼmenemo. Adzawononga mzinda ndi onse okhalamo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kumina kwa akavalo ace kunamveka ku Dani; dziko lonse linanthunthumira pa kulira kwa akavalo acewo olimba; cifukwa afika, nadya dziko ndi zonse za momwemo; mudzi ndi amene akhalamo.