Jeremiah 8:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Imvani kulira kwa anthu anga kuchokera ku dziko lakutali. Akuti, “Kodi Chauta sali ku Ziyoni? Kodi mfumu yake siili kumeneko?” Chauta ayankha kuti, “Chifukwa chiyani akundiputa ndi mafano ao, ndiponso ndi milungu yao yachilendo?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, mau a kulira kwa mwana wamkazi wa anthu anga ochokera kudziko lakutali: Kodi m'Ziyoni mulibe Yehova? Kodi mulibe mfumu yake? Chifukwa chanji andiputa Ine ndi mafano ao osema, ndi zachabe zachilendo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Imvani kulira kwa anthu anga kuchokera ku dziko lakutali: akuti, “Kodi Yehova sali ku Ziyoni? Kodi mfumu yake sili kumeneko?” “Chifukwa chiyani akundiputa ndi mafano awo osema, ndi milungu yawo yachilendo?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, mau a kulira kwa mwana wamkazi wa anthu anga ocokera ku dziko lakutari: Kodi m'Ziyoni mulibe Yehova? Kodi mulibe Mfumu yace? Cifukwa canji andiputa Ine ndi mafano ao osema, ndi zacabe zacilendo?