Jeremiah 8:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzaŵamwaza pa mtunda kuyang'ana mwezi, ndi nyenyezi zonse zakumwamba zimene ankazikonda, kumazitumikira, kuzitsata, kuzipempha nzeru ndi kumazipembedza. Mafupa amenewo sadzaŵasonkhanitsa kapena kuŵakwirira, koma adzasanduka ndoŵe pamwamba pa nthaka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo udzawayanika padzuwa, ndi pamwezi, ndi pa khamu lonse la kuthambo, limene analikonda, ndi kulitumikira, ndi kulitsata, ndi kulifuna, ndi kuligwadira; sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ndowe panthaka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adzawamwaza pa nthaka kuyangʼana dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zonse zamlengalenga, zimene ankazikonda, kuzitumikira ndi kuzitsatira, kupemphako nzeru ndiponso kuzilambira. Mafupawo sadzawasonkhanitsa kapena kuwakwirira, koma adzakhala ngati ndowe pamwamba pa nthaka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika