Jeremiah 8:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adandiwuza kuti ndifunse anthu ake mau aŵa: “Kodi anthu akagwa, ndiye kuti sangathe kudzukanso? Kodi munthu akasokera, ndiye kuti sangathe kubwereranso?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso udzati kwa iwo, Atero Yehova, Kodi adzagwa, osaukanso? Kodi wina adzachoka, osabweranso?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono awuze anthuwa, ‘Yehova akuti: “ ‘Kodi anthu akagwa sangadzukenso? Munthu akasochera kodi sangathe kubwereranso?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso udzati kwa iwo, Atero Yehova, Kodi adzagwa, osaukanso? Kodi wina adzacoka, osabweranso?