Jeremiah 8:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndakhala ndikutchereza ndi kuŵamvetsera, koma sadalankhulepo zoona. Palibe wochimwa aliyense amene adandiwonetsa kuti walapa, namanena kuti, ‘Ndachitanji ine?’ Koma aliyense akungotsata njira zake, ngati kavalo wothamangira nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinatchera khutu, ndinamva koma sananene bwino; panalibe munthu amene anatembenuka kusiya zoipa zake, ndi kuti, Ndachita chiyani? Yense anatembenukira njira yake, monga akavalo athamangira m'nkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndinatchera khutu kumvetsera koma iwo sanayankhulepo zoona. Palibe woyipa amene analapapo zoyipa zake, nʼkumati, ‘Ine ndachita chiyani?’ Aliyense akutsatira njira yake ngati kavalo wothamangira nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinachera khutu, ndinamva koma sananena bwino; panalibe munthu amene anatembenuka kusiya zoipa zace, ndi kuti, Ndacita ciani? yense anatembenukira njira yace, monga akavalo athamangira m'nkhondo.