Jeremiah 8:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mbalame amati kapande ija imadziŵa nthaŵi yake mumlengalenga. Nkhunda, namzeze ndi ngalu zimadziŵa nthaŵi yake yonyamukira ulendo. Koma anthu anga sadziŵa malangizo a Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inde, chumba cha mlengalenga chidziwa nyengo zake; ndipo njiwa ndi namzeze ndi chingalu ziyang'anira nyengo yakufika kwao; koma anthu anga sadziwa chiweruziro cha Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mbalame yotchedwa kakowa ija imadziwa nthawi yake mlengalenga. Koma nkhunda, namzeze ndi chingalu zimadziwa nthawi yonyamukira ulendo, koma anthu anga sadziwa malamulo a Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inde, cumba ca mlengalenga cidziwa nyengo zace; ndipo njiwa ndi namzeze ndi cingaru ziyang'anira nyengo yakufika kwao; koma anthu anga sadziwa ciweruziro ca Yehova.