Jeremiah 9:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndidati, “Ndidzamva chisoni ndi kulira mokweza chifukwa cha mapiri. Ndidzadandaula chifukwa cha mabusa am'chipululu popeza kuti malo onsewo aonongeka. Palibe amene amapitako, sikumveka nkulira kwa ng'ombe komwe. Mbalame zonse zouluka ndiponso nyama zakuthengo zathaŵa, osaonekanso.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa cha mapiri ndidzagwa misozi ndi kulira, chifukwa cha mabusa a chipululu ndidzachita maliro, chifukwa apserera, kuti anthu sangathe kupitirirapo; ndiponso anthu sangathe kumva mau a ng'ombe zao; mbalame za mlengalenga ndi nyama zathawa, zapita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzakhetsa misozi ndi kulira kwamphamvu chifukwa cha mapiri ndipo ndidzadandaula chifukwa cha msipu wa ku chipululu. Malo onsewo awonongeka ndipo palibe amene amapitako, ndipo sikumveka kulira kwa ngʼombe. Mbalame zamlengalenga zathawa ndipo nyama zakuthengo zachokako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa ca mapiri ndidzagwa misozi ndi kulira, cifukwa ca mabusa a cipululu ndidzacita maliro, cifukwa apserera, kuti anthu sangathe kupitirirapo; ndiponso anthu sangathe kumva mau a ng'ombe zao; mbalame za mlengalenga ndi nyama zathawa, zapita.