Jeremiah 9:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndidati, “Kodi wanzeru ndani, amene angamvetse zimenezi? Chauta adazifotokozera yani, kuti iyeyo akafotokozere ena? Nanga chifukwa chiyani dziko laonongeka ndi kusanduka chipululu, m'mene anthu sapitamo?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wanzeru ndani, kuti adziwe ichi? Ndani iye amene kamwa la Yehova lanena naye, kuti achilalikire? Chifukwa chake dziko litha ndi kupsereza monga chipululu, kuti anthu asapitemo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndinati, “Kodi munthu wanzeru ndani woti nʼkumvetsa zimenezi? Kodi ndani amene Yehova anayankhula naye zimenezi kuti akafotokozere ena? Nʼchifukwa chiyani dziko lawonongeka ndi kusanduka chipululu, mʼmene anthu sadutsamo?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wanzeru ndani, kuti adziwe ici? ndani iye amene kamwa la Yehova lanena naye, kuti acilalikire? cifukwa cace dziko litha ndi kupserera monga cipululu, kuti anthu asapitemo?