Jeremiah 9:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tamvani tsono zimene Ine Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, ndidzachite. Anthu ameneŵa ndidzaŵadyetsa ziphe ndi kuŵamwetsa madzi azumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Taonani, ndidzadyetsa anthu awa chivumulo, ndi kuwamwetsa madzi andulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono chimene Ine Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli ndidzachite ndi anthu amenewa ndi ichi: “Ndidzawadyetsa chakudya cha ziphe ndi kuwamwetsa madzi a ndulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Taonani, ndidzadyetsa anthu awa civumulo, ndi kuwamwetsa madzi andulu.