Jeremiah 9:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Muziganize bwino, muitane akazi olira maliro kuti abwere. Akaziwo akhale aja amadziŵa kwambiri kuliraŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova wa makamu, Kumbukirani inu, ndi kuitana akazi akulira, adze; aitaneni akazi ochenjera, kuti adze;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Tsopano ganizirani! Muyitane akazi olira mwachisoni kuti abwere; itanani akazi odziwa kulira bwino.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova wa makamu, Kumbukirani inu, ndi kuitana akazi akulira, adze; aitaneni akazi ocenjera, kuti adze;