Jeremiah 9:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndidati, “Inu azimai, mverani mau a Chauta. Tcherani makutu kuti mumve zimene akunena. Ana anu aakazi muŵaphunzitse kulira. Aliyense aphunzitse mnzake nyimbo yamaliro.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma imvani mau a Yehova, akazi inu, khutu lanu lilandire mau a pakamwa pake, phunzitsani ana anu akazi kulira, ndi yense aphunzitse mnzake maliridwe ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono inu amayi, imvani mawu a Yehova; tcherani makutu anu kuti mumve mawu a Yehova. Phunzitsani ana anu aakazi kulira mwachisoni; aliyense aphunzitse mnzake nyimbo ya maliro.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma imvani mau a Yehova, akazi inu, khutu lanu lilandire mau a pakamwa pace, phunzitsani ana anu akazi kulira, ndi yense aphunzitse mnzace maliridwe ace.