Jeremiah 9:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adandiwuza kuti ndinene izi: “Mitembo ya anthu idzagwa, kuchita kuti mbwembwembwe ngati ndoŵe m'minda, ngati mitolo pambuyo pa anthu ovuna. Koma palibe amene adzaitole.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nenani, atero Yehova, Mitembo yathu idzagwa ngati ndowe pamunda, ndi monga chipukutu pambuyo pa wakusenga, palibe wochitola.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anandiwuza kuti ndinene izi kuti, “ ‘Mitembo ya anthu idzakhala ili lambalamba ngati ndowe mʼminda, ngati mapesi mʼmbuyo mwa wokolola, popanda munthu woyitola.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nenani, atero Yehova, Mitembo yathu idzagwa ngati ndowe pamunda, ndi monga cipukutu pambuyo pa wakusenga, palibe wocitola.