Jeremiah 9:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amapinda lilime ngati uta. Dziko ladzaza ndi zabodza osati zoona. “Amanka naonjezeraonjezera zoipa, ndipo sandidziŵa Ine,” akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo apinda lilime lao ngati uta wao, liname; koma akula mphamvu m'dzikomo, koma si pachoonadi; pakuti alinkunkabe nachita zoipa, ndipo sandidziwa Ine, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Amapinda lilime lawo ngati uta. Mʼdzikomo mwadzaza ndi mabodza okhaokha osati zoonadi. Amapitirirabe kuchita zoyipa; ndipo sandidziwa Ine.” Akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo apinda lilime lao ngati uta wao, liname; koma akula mphamvu m'dzikomo, koma si pacoonadi; pakuti alinkunkabe nacita zoipa, ndipo sandidziwa Ine, ati Yehova.