Jeremiah 9:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aliyense amanyenga mnzake, ndipo sanena zoona. Pakamwa pao adapazoloŵeza kulankhula zonama. Amakonda zoipa kwambiri, kotero kuti sangathenso kulapa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo yense adzanyenga mnansi wake, osanena choonadi; aphunzitsa lilime lao kunena zonama; nadzithodwetsa kuchita zoipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense amamunamiza mʼbale wake ndipo palibe amene amayankhula choonadi. Anapazoloweza pakamwa pawo kunena zabodza; amalimbika kuchita machimo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo yense adzanyenga mnansi wace, osanena coonadi; aphunzitsa lilime lao kunena zonama; nadzithodwetsa kucita zoipa.