Jeremiah 9:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Lilime lao lili ngati muvi wakuthwa. Aliyense pakamwa pake pamatuluka mau aubwenzi, m'menemo mumtima mwake akukonzekera zomchita mnzake chiwembu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Lilime lao ndi muvi wakuphera; linena manyengo; wina anena mtendere ndi mnansi wake pakamwa pake, koma m'mtima mwake amlalira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lilime lawo lili ngati muvi wakuthwa; limayankhula zachinyengo. Aliyense ndi pakamwa pake amayankhula mawu achikondi kwa mnansi wake, koma mu mtima mwake amakonzekera zomuchita chiwembu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Lilime lao ndi mubvi wakuphera; linena manyengo; wina anena mtendere ndi mnansi wace pakamwa pace, koma m'mtima mwace amlalira.