Job 1:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Suja Inu mwakhala mukumteteza ponseponse iye uja, pamodzi ndi banja lake ndi zinthu zake zonse zimene ali nazo. Mudamdalitsanso pa ntchito zimene amachita, ndipo chuma chake nchochuluka kwambiri m'dzikomo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi simunamtchinga iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pomzinga ponse? Ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoweta zake zachuluka m'dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kodi Inu simumamuteteza iyeyo, nyumba yake ndi zonse zimene ali nazo? Mwadalitsa ntchito ya manja ake, kotero kuti nkhosa ndi ngʼombe zake zili ponseponse mʼdzikomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi simunamcinga iye ndi nyumba yace, ndi zace zonse, pomzinga ponse? nchito ya manja ace mwaidalitsa, ndi zoweta zace zacuruka m'dziko.