Job 1:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yobe atamva zimenezo, adadzambatuka, nkung'amba zovala zake. Adameta tsitsi, ndipo adadzigwetsa pansi napembedza Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Yobu ananyamuka, nang'amba malaya ake, nameta mutu wake, nagwa pansi, nalambira,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atamva zimenezi, Yobu anayimirira nangʼamba mkanjo wake, ndi kumeta tsitsi lake. Kenaka anadzigwetsa pansi napembedza Mulungu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Yobu ananyamuka, nang'amba maraya ace, nameta mutu wace, nagwa pansi, nalambira,