Job 1:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adati, “M'mimba mwa amai ndidatulukamo maliseche, namonso m'manda ndidzaloŵamo maliseche, Chauta ndiye adapatsa, Chauta ndiyenso walanda. Litamandike dzina la Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nati, Ndinatuluka m'mimba ya mai wanga wamaliseche, wamaliseche ndidzamukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
nati, “Ndinatuluka maliseche mʼmimba mwa amayi anga, namonso mʼmanda ndidzalowa wamaliseche. Yehova ndiye anapereka ndipo Yehova watenga; litamandike dzina la Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nati, Ndinaturuka m'mimba ya mai wanga wamarisece, wamarisece ndidzanrukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.