Job 1:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anali ndi nkhosa 7,000, ngamira 3,000, ng'ombe zantchito 1,000 ndi abulu aakazi 500. Anali ndi antchito ambiri, choncho anali munthu wotchuka koposa anthu onse a m'maiko akuvuma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zoweta zakenso zinali nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi ngamira zikwi zitatu, ndi ng'ombe zamagoli mazana asanu, ndi abulu akazi mazana asanu, antchito ake omwe ndi ambiri; chotero munthuyu anaposa anthu onse a kum'mawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo anali ndi nkhosa 7,000, ngamira 3,000, ngʼombe zantchito 1,000 ndi abulu aakazi 500, ndiponso anali ndi antchito ambiri. Iye anali munthu wotchuka kwambiri pakati pa anthu onse a mʼmayiko a kummawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zoweta zacenso zinali nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi ngamila zikwi zitatu, ndi ng'ombe zamagoli mazana asanu, ndi aburu akazi mazana asanu, anchito ace omwe ndi ambiri; cotero munthuyu anaposa anthu onse'a kum'mawa.