Job 1:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono masiku a phwandowo akatha, Yobe ankadzuka m'mamaŵa napereka nsembe, kuperekera mwana aliyense, kuti anawo ayeretsedwe potsata malamulo a chipembedzo. Yobeyo ankati, “Mwina mwake, wina mwa ana angaŵa adachimwa, adatukwana Mulungu mumtima mwake.” Umu ndimo m'mene ankachitira Yobe nthaŵi zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunatero, atatha masiku a madyererowa Yobu anatumiza mau, nawapatula, nauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, monga mwa kuwerenga kwa iwo onse; pakuti Yobu anati, Kapena anachimwa ana anga, nachitira Mulungu mwano m'mtima mwao, Anatero Yobu masiku onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Masiku aphwandowo atatha, Yobu ankawayitana kuti adzawayeretse. Mmamawa iye ankapereka nsembe yopsereza kuperekera mwana aliyense, poganiza kuti, “Mwina ana anga achimwa ndi kutukwana Mulungu mʼmitima yawo.” Umu ndi mmene Yobu ankachitira nthawi zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunatero, atatha masiku a madyererowa Yobu anatumiza mau, nawapatula, nauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, monga mwa kuwerenga kwa iwo onse; pakuti Yobu anati, Kapena anacimwa ana anga, nacitira Mulungu mwano m'mtima mwao. Anatero Yobu masiku onse.