Job 14:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masiku a munthu ndi oŵerengeka, chiŵerengero cha miyezi yake mumachidziŵa ndinu. Inu mudamulembera malire ake, sangathe kuŵalumpha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza masiku ake alembedwa, chiwerengo cha miyezi yake chikhala ndi Inu, ndipo mwamlembera malire ake kuti asapitirirepo iye;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Masiku a munthu ndi odziwikiratu; munakhazikitsa chiwerengero cha miyezi yake ndipo munamulembera malire amene sangathe kuwalumpha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza masiku ace alembedwa, ciwerengo ca miyezi yace cikhala ndi Inu, Ndipo mwamlembera malire ace, kuti asapitirirepo iye;