Job 16:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaali pa mtendere, koma Mulungu adanditswanya. Adandigwira pa khosi ndi kundiphwanya. Adandiimika kuti ndikhale choponyerapo chandamale chake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinali mkupuma, koma anandithyola; inde anandigwira pakhosi, nandiphwanya; nandiimika ndikhale chandamali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndinali pamtendere, koma Mulungu ananditswanya; anandigwira pa khosi ndi kundiphwanya. Iye anandisandutsa choponyera chandamale chake;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinali mkupuma, koma anandityola; Inde anandigwira pakhosi, nandiphwanya; Anandiimika ndikhale candamali.