Job 18:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe ukungodzipweteka ndi mkwiyo wako. Kodi dziko lapansi lidzasanduka bwinja chifukwa choti iweyo uli wokwiya? Kodi thanthwe nkudzachotsedwa pamalo pake, kuti likukondweretse iweyo?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwe wodzing'amba mumkwiyo mwako, kodi dziko lapansi lisiyidwe chifukwa cha iwe? Kapena thanthwe lisunthike m'malo mwake?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe amene ukudzipweteka wekha ndi mkwiyo wako, kodi dziko lapansi lisanduke bwinja chifukwa cha iweyo? Kodi kapena thanthwe lisunthidwe kuchoka pa malo ake?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwe wodzing'amba mumkwiyo mwako, Kodi dziko lapansi lisiyidwe cifukwa ca iwe? Kapena thanthwe lisunthike m'malo mwace?