Job 2:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yobe adauza mkazi wakeyo kuti, “Ukulankhula ngati mkazi wopusa. Ngati tilandira zokondweretsa kwa Mulungu, tilekerenji kulandiranso zoŵaŵa?” Motero pa zonsezi Yobe sadachimwe polankhula pake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ananena naye, Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! Tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa? Pa ichi chonse Yobu sanachimwe ndi milomo yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yobu anayankha kuti, “Ukuyankhula ngati mkazi wopusa. Kodi tidzalandira zokoma zokhazokha kwa Mulungu, osalandiranso zowawa?” Mu zonsezi, Yobu sanachimwe pa zimene anayankhula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ananena naye, Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa? pa ici conse Yobu sanacimwa ndi milomo yace.